kodi aneneri a Mulungu awa Abrahamu,Mose,Yesu ndi Muhammad (madalitso ndi mtendere wa mulungu zikhale pa iwo) ankapembeza bwanji?
Nthawi ina yake Sheikh Ahmed Deedat, amene ali womphunzira wachisilamu wankulu adayendera m’dzinda wa Jeddah womwe ukupezeka mu dziko la Saudi Arabia ndipo Sheikhewa adatilongosolera ife zina mwa zinthu zomwe zidawachitikira pa umoyo wawo.
Iwo adati tsiku lina adatenga gulu la Akristu ndi Ayuda kuti akaone m’zikiti winawake mwa mizikiti ya mudzinda wa Durban m’dziko la South Africa. Ndipo panthawi yomwe adalowa mu m’zikiti Deedat sanangovula nsapato yekha ayi koma adaliwuzanso gulu lija kuti nalo livule nsapato ndipo gululo linamvera ndikuchita chimodzimodzi.
Ndipo Mose ndi Aaroni ndi ana ace amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m’menemo;32 pakulowa iwo m’chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la msembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.(Eksodo 40:31-32)
Pambuyo poti Sheikh Deedat apemphera swalat yokakamizidwa(Faradhwi) anapitanso ku gulu lomwe anabwera nalo lija lomwe panthawiyi linali ndi chidwi kwambiri kuyang’ana asilamu ena mu m’zikitimu omwe amapemphera mapemphero ongozipereka(omwe amatchedwa kuti ma sunnah). Anayamba kulilongosolera gululi kakhalidwe kosiyanasiyana komwe amachita munthu amene akupemphera, maka kugwetsa nkhope pansi. Sheikh Deedat anasindika mawu ake ponena kuti ndithu kugwetsa nkhope pansiku ndikomwenso aneneri onse amachita pamapemphero awo. Adasindikanso mawuwa popereka maumboni nati:
Ndipo Mose ndi Aaroni anachoka pamalo pa msonkhano kumka ku khomo la cihema cokomanako,nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo. (Numeri 20:6)